Hosea 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaononga mitengo yake yamphesa ndi yankhuyu imene ankanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo malipiro anga amene zibwenzi zanga zidandipatsa.’ Ndidzaisandutsa malunje, ndipo zilombo zizidzadya kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama za kuthengo zidzaidya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu, imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake. Ndidzayisandutsa chithukuluzi, ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapasula mipesa yace ndi mikuyu yace, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.