Hosea 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko ndidzambwezera minda yake yamphesa. Ndidzasandutsa Chigwa cha Mavuto kuti chikhale chipata cha kuchiyembekezo. Ndipo kumeneko azidzandiyankha monga m'mene ankandiyankhira pa ubwana wake, atatuluka ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzampatsa minda yake yamphesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa, ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo. Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake, monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzampatsa minda yace yamphesa kuyambira pomwepo, ndi cigwa ca Akori cikhale khomo la ciyembekezo; ndipo adzabvomereza pomwepo monga masiku a ubwana wace, ndi monga tsiku lokwera iye kuturuka m'dziko la Aigupto.