Hosea 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga. Ndidzachotsa mʼdzikomo uta, lupanga ndi zida zonse zankhondo, kuti onse apumule mwamtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lomwelo ndidzawacitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzatyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zicoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.