Hosea 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Israele ndidzamubzala m'dziko kuti akhale wanga. Ndidzaonetsa chikondi kwa ‘Sakondedwa’ uja. Anthu amene ndinkaŵatchula ‘Si-anthu-anga,’ ndidzaŵauza kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Ndinu Mulungu wathu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga: ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’ Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’ ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzacitira cifundo Wosacitidwa-cifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.