Hosea 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akapanda kutero ndimuvula, kuti akhale monga momwe adabadwira. Ndidzamuumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndidzamphetsa ndi ludzu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akapanda kutero ndidzamuvula, ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa; ndidzamuwumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndi kumupha ndi ludzu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndingambvule wamarisece, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati cipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;