Hosea 2:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mai wao ndi wachiwerewere. Amene adaŵabala ankachita zomvetsa manyazi. Ankati, ‘Nditsatira zibwenzi zanga zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi vinyo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi. Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga, zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mai wao anacita cigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anacita camanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine cakudya canga, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi cakumwa canga.