Hosea 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzathamangira zibwenzi zake, koma sadzapezana nazo. Adzazifunafuna, koma osazipeza. Tsono adzati, ‘Ndibwereranso kwa mwamuna wanga uja, chifukwa ndidaali pabwino ndi iyeyo kupambana tsopano.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza; adzazifunafuna koma sadzazipeza. Pamenepo iye adzati, ‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja, pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzatsata omkonda koma osawakumika, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano.