Hosea 2:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanazindikire kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta. Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide, zimene ankapangira mafano a Baala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumcurukitsira siliva ndi golidi, zimene anapanga nazo Baala.