Hosea 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Pitanso, ukakonde mkazi wachigololo amene ali ndi chibwenzi chake. Umkonde monga momwe Ine Chauta ndimakondera Israele, ngakhale iyeyo amapembedza milungu ina, ndipo amakonda kuitsirira nsembe za mphesa zabwino zoumika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lace, koma wakucita cigololo monga Yehova akonda ana a Israyeli, angakhale atembenukira ku milungu yina, nakonda ncinci za mphesa zouma.