Hosea 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti Aisraele adzakhala masiku ambiri opanda mafumu kapena akalonga, osapereka nsembe kapena kuimika miyala yachipembedzo, opanda zamaula kapena mafano oombezera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana Israyeli adzakhala masiku ambiri a opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda coimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;