Hosea 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Aisraele, imvani mau a Chauta, chifukwa Iye akukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'dziko. Mlandu wake ndi wakuti, m'dziko mulibe kukhulupirika kapena kukoma mtima, ndipo Mulungu samulabadira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova, chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu amene mumakhala mʼdzikoli: “Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi mulibe kulabadira za Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani mau a Yehova, inu ana a Israyeli; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe coonadi, kapena cifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.