Hosea 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi miniali, ndi mkundi; popeza mthunzi wace ndi wabwino, cifukwa cace ana anu akazi acita citole, ndi apongozi anu acita cigololo.