Hosea 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindidzalanga ana anu akazi pocita citole iwo, kapena apongozi anu pocita cigololo iwo; pakuti iwo okha apambukira padera ndi akazi acitole, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa kucitole; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa camutu.