Hosea 4:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngakhale Aisraele amachita zosakhulupirika, anthu a ku Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. Asapite kukapembedza ku Giligala kapena ku Betehaveni. Asakalumbirenso kumeneko kuti, ‘Pali Chauta wamoyo!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli, Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. “Usapite ku Giligala. Usapite ku Beti-Aveni. Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinkana iwe, Israyeli, ucita citole, koma asaparamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.