Hosea 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake mudzagwa chilala m'dziko, ndipo onse okhalamo adzavutika pamodzi ndi nyama zakuthengo zomwe, ndi mbalame zamumlengalenga. Ngakhale nsomba zam'nyanja zidzafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chake dziko likulira ndipo onse amene amakhalamo akuvutika; zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace dziko lidzacita cisoni, ndi ali yense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzacotsedwa.