Hosea 5:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ansembe inu, imvani izi! Aisraele inu, mumvetsere nonse. Inu a m'banja la mfumu, mvetserani mau anga. Chilango chidzakugwerani, chifukwa inu munali msampha ku Mizipa, mudachita ngati kuyala ukonde ku phiri la Tabori.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ansembe inu, imvani izi! Inu Aisraeli, tcherani khutu! Inu nyumba yaufumu, mvetserani! Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu: Inu munali ngati msampha ku Mizipa, munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani ici, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israyeli; cherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti ciweruzoci cinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabora.