Hosea 5:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono anthu a ku Efuremu ataona kuti akudwala, ndipo Ayuda ataona kuti ali ndi mabala, Aefuremuwo adapita kwa Aasiriya, Ayuda natuma uthenga kwa mfumu yaikulu, kuti iŵathandize. Koma siingathe kuŵachiritsa kapena kupoletsa mabala ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Efereimu ataona nthenda yake, ndi Yuda ataona zilonda zake, pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya, ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza. Koma mfumuyo singathe kukuchizani, singathe kuchiritsa mabala anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Efraimu anaona nthenda yace, ndi Yuda bala lace, Efraimu anamuka kwa Asuri, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuciritsani, kapena kupoletsa bala lanu.