Hosea 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalumphira Aefuremu ngati mkango, ndidzambwandira Ayuda ngati msona wa mkango. Ine mwini ndidzaŵakadzula nkuchokapo. Pamene ndizidzaŵaguza, palibe wina aliyense wotha kudzaŵalanditsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu. Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda. Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo; ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzakhala kwa Efraimu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kucoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.