Hosea 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzabwerera ku malo anga, mpaka anthu anga atasaukiratu, ndi kuyamba kundifunafuna. M'mavuto ao adzayesetsa kundipeza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndidzabwerera ku malo anga mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo. Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga; mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzamuka ndi kubwerera kumka kumalo kwanga, mpaka adzabvomereza kuparamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwacangu.