Hosea 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amapereka nsembe zankhosa ndi zang'ombe pofunafuna Chauta, koma samupeza, waŵachokera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo kukapereka nsembe kwa Yehova, iwo sadzamupeza; Iye wawachokera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikuru kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwacokera.