Hosea 5:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imbani malipenga ankhondo ku Gibea! Lizani mbetete ku Rama! Chenjezani a ku Betehaveni! Inu a ku Benjamini tsogolani!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ombani mphalasa m'Gibea, ndi lipenga m'Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Womba lipenga mu Gibeya, liza mbetete mu Rama. Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni; iwe Benjamini tsogolera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ombani mphalasa m'Gibeya, ndi lipenga m'Rama; pfuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini.