Hosea 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta akuti, “Inu Aefuremu, kodi ndikuchiteni chiyani? Nanga inu Ayuda, ndikuchiteni chiyani? Chikondi chanu chimazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, chili ngati mame okamuka msanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani? Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda? Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa, ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Efraimu iwe, ndidzakucitira ciani? Yuda iwe, ndikucitire ciani? pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.