Hosea 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndakuŵazani ngati nkhuni ndi machenjezo a aneneri, ndakuphani ndi mau anga. Chigamulo changa nchoonekeratu ngati kuŵala kwa dzuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga, ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga; chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga aturuka ngati kuunika.