Hosea 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga mbala zimalalira munthu, momwemonso ansembe amasonkhana kuti azipha anthu pa njira ya ku Sekemu. Zoonadi amachita zachifwamba zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi acita coipitsitsa.