Hosea 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine. Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira. Ndimafuna kuŵapulumutsa, koma amangolankhula zabodza za Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa iwo, chifukwa andisiya Ine! Chiwonongeko kwa iwo, chifukwa andiwukira! Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa koma amayankhula za Ine monama.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iwowa! pakuti anandizembera; cionongeko kwa iwowa! pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.