Hosea 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulira kwao kwa Ine nkwabodza, amalira ali gone pa bedi. Amadzichekacheka ngati akunja chifukwa chofuna chakudya ndi chakumwa, komabe amandipandukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima, koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo. Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano, koma amandifulatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanapfuulira kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.