Hosea 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amatembenukira kwa mulungu wachabechabe, osati kwa Mulungu wopambanazonse. Ali ngati uta wokhota. Atsogoleri ao adzaphedwa ndi lupanga chifukwa chakuti amandilankhulira zachipongwe. Motero a ku Ejipito adzaŵaseka kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba; ali ngati uta woonongeka. Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga chifukwa cha mawu awo achipongwe. Motero iwo adzasekedwa mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa cipongwe ca lilime lao; ici ndico adzawasekera m'dziko la Aigupto.