Hosea 8:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amapereka nsembe zanyama kwa Ine nkumadya, koma Ine Chauta sindikondwera nazo konse. Sindidzaiŵala zolakwa zao, ndidzaŵalanga chifukwa cha zimenezo. Ndidzaŵabwezera ku ukapolo ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amapereka nsembe za nyama kwa Ine ndipo iwo amadya nyamayo, koma Yehova sakondwera nazo. Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo: iwowo adzabwerera ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukila mphulupulu yao, nadzalanga zocimwa zao; adzabwerera kumka ku Aigupto.