Hosea 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adzimangira nyumba zikuluzikulu, kuiŵala Mlengi wao. Ayuda achulukitsa mizinda yamalinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yaoyo, ndipo motowo udzatentha nyumba zao zazikuluzo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli wayiwala Mlengi wake ndipo wamanga nyumba zaufumu; Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo, moto umene udzatenthe malinga awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Israyeli waiwala Mlengi wace, namanga akacisit ndipo Yuda wacurukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yace moto, nudzatha nyumba zace zazikuru.