Hosea 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Fano la mwanawang'ombe limene a ku Samariya akupembedza likundinyansa. Motero mkwiyo wanga waŵayakira kwambiri anthuwo. Padzapita nthaŵi yaitali chotani asanasinthe kuti ayere anthu a ku Israele?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe! Mkwiyo wanga wayakira anthuwo. Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana wa ng'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?