Hosea 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Fanolo si mulungu konse, adalipanga ndi munthu waluso. Fano la ku Samariyali lidzatswanyidwa pafupipafupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ici comwe cafumira kwa Israyeli; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwana wa ng'ombe wa Samariya adzaphwanyika-phwanyika.