Hosea 8:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aisraele amafesa kamphepo, ndipo amakolola kamvulumvulu. Tirigu alibe ngala, sadzabala chakudya. Akadabala, alendo akadadya chakudyacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aisraeli amadzala mphepo ndipo amakolola kamvuluvulu. Tirigu alibe ngala; sadzabala chakudya. Akanabala chakudya alendo akanadya chakudyacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.