Hosea 8:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adathaŵira ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera payokha. Aefuremu adalipira anthu a ku maiko ena kuti akhale oŵathandiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anakwera kumka ku Asuri, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wace; Efraimu walembera omkonda ngati anchito.