Hosea 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musakondwere Aisraele inu! Musakhale ndi chisangalalo chonga cha mitundu ina ya anthu. Mwasiya Mulungu wanu monga amachitira mkazi wosakhulupirika. Mwadzigulitsa kwa Baala ngati mkazi wadama, kuti mukalandireko zokolola zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Israeli, usakondwere; monga imachitira mitundu ina. Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako; umakonda malipiro a chiwerewere pa malo aliwonse opunthira tirigu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usakondwera, Israyeli, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wacita cigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya cigololo pa dwale la tirigu liri lonse.