Hosea 9:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo. Makolo ake aja ndidaŵakondwerera ngati nkhuyu zoyamba kupsa. Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori, ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala. Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo, limene ankalikonda lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene ndinamupeza Israeli zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu. Nditaona makolo anu, zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma atafika ku Baala Peori, anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinapeza Israyeli ngati mphesa m'cipululu, ndinaona makolo anu ngati cipatso coyamba ca mkuyu nyengo yace yoyamba; koma anadza kwa Baala Peori, nadzipatulira conyansaco, nasandulika onyansa, conga cija anacikonda.