Hosea 9:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Kuipa kwao konse kudaoneka makamaka ku Giligala. Ndidayamba kudana nawo kumeneko. Ndidzaŵapirikitsa m'dziko mwanga, chifukwa makhalidwe ao ndi oipa. Sindidzaŵakondanso, atsogoleri ao onse andiwukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Choipa chao chonse chili m'Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala, Ine ndinawada kumeneko. Chifukwa cha machitidwe awo auchimo, ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga. Sindidzawakondanso; atsogoleri awo onse ndi owukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Coipa cao conse ciri m'Giligala; pakutipamenepo ndinawada, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe ao ndidzawainga kuwacotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.