Hosea 9:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumeneko anthu sadzaperekanso zopereka za chakumwa kupereka kwa Chauta. Sadzamkondwetsanso ndi nsembe zao. Chakudya chao chidzakhala ngati chakudya chapamaliro, onse amene adzadya chakudya chimenecho adzaipitsidwa. Chakudyacho chidzangokhala chodyera njala chabe, osati choti nkukapereka ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova, kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo. Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa; onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa. Chakudya ichi chidzakhala chodya okha, sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa acisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumbaya Yehova.