Hosea 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ya chilango ikadzafika, iwo nkubalalika, Aejipito adzaŵakusa, nakaŵaika m'manda komweko ku Memfisi. Khwisa adzamera pa ziŵiya zao zasiliva. M'nyumba mwao mudzamera minga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko, Igupto adzawasonkhanitsa, ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda. Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva, ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, anacokera cionongeko, koma Aigupto adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.