Hosea 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ya chilango yafikadi, masiku olipsira aŵagwera. Pamenepo adzadziŵa kuti zimenezi nzoonadi. Tsopano akunena kuti, “Mneneriyu nchitsilu, munthu wa nzeru za kwa Mulunguyu ndi wamsala!” Amatero chifukwa zolakwa zao zachuluka, chidani chao nchachikulukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku achilango akubwera, masiku obwezera ali pafupi. Israeli adziwe zimenezi. Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri. Mneneri amamuyesa chitsiru, munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israyeli adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, cifukwa ca kucuruka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukuru.