Hosea 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mneneri ndiye wochenjeza Aefuremu, anthu a Mulungu wanga. Koma mneneriyo amtchera msampha m'njira zake zonse, ndipo adani akumlalira m'Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga ndiwo alonda a Efereimu, koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse, ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Efraimu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zace zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wace.