Isaiah 1:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.