Isaiah 1:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Tamvera, iwe mlengalenga, tchera khutu, iwe dziko lapansi, Ine Chauta ndikulankhula. Ndidabereka ana ndi kuŵalera, koma andigalukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, cifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.