Isaiah 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani momwe mzinda wokhulupirika wasandukira wadama! Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama; mu mzindamo munali chilungamo, koma tsopano muli anthu opha anzawo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.