Isaiah 1:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, Wamphamvu uja wa Israele, akunena kuti: “Ha! Olimbana nane ndidzaŵatha, adani anga ndidzaŵalipsira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu, Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti, “Haa, odana nane ndidzawatha, ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli, Ha! ndidzatonthoza mtima wanga pocotsa ondibvuta, ndi kubwezera cilango adani anga;