Isaiah 1:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aweruzi ako ndidzaŵakhazikitsanso ngati pa masiku akale aja. Aphungu akonso ndidzaŵakhazikitsanso ngati poyamba paja. Pambuyo pake iweyo udzatchedwa mzinda waungwiro, mzinda wokhulupirika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana, aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja. Kenaka iweyo udzatchedwa mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga paciyambi; pambuyo pace udzachedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.