Isaiah 1:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amphamvu adzasanduka ngati udzu wouma, ntchito zao ngati mbaliŵali. Motero anthuwo adzayakira limodzi ndi ntchito zaozo, popanda woti auzimitse motowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma, ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali; motero zonse zidzayakira limodzi, popanda woti azimitse motowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndimo wamphamvu adzakhala ngati cingwe cabwazi, ndi nchito yace ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.