Isaiah 1:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ha, mtundu wochimwa, inu anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoipa, ana omira m'zoipa! Mudasiya Chauta, mudanyoza Woyera uja wa Israele, mudamufulatira kwathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Haa, mtundu wochimwa, anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoyipa, ana odzipereka ku zoyipa! Iwo asiya Yehova; anyoza Woyerayo wa Israeli ndipo afulatira Iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtundu wocimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakucita zoipa, ana amene acita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.