Isaiah 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu aitentha. Alendo akukuwonongerani dziko inu muli pomwepo. Lasanduka bwinja, lagonjetsedwa ndi alendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lanu lili bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; minda yanu ikukololedwa ndi alendo inu muli pomwepo, dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lanu liri bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo liri labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.