Isaiah 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzinda wa Yerusalemu watsala wokhawokha ngati nsanja m'munda wamphesa, ngati dinda m'munda wa minkhaka, ngatinso mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wamphesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha ngati nsanja mʼmunda wampesa, ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati citando ca m'munda wamphesa, ngati cilindo ca m'munda wamankhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.