Isaiah 10:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha nchito yace yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asuri, ndi ulemerero wa maso ace okwezedwa.